制作
出演艺人
Sir Paul Banda
表演者
作曲和作词
Sir Paul Banda
词曲作者
Lucius Banda
作曲
制作和工程
Sir Paul Banda
制作人
歌词
Mulungu adalenga munthu
Ndi zonse zosangalatsa kale
Malemba ati anawona
Kuti zonse zinali bwino ndithu
Anamupatsa munthu mawu
Kuti choncho asangalale ndi kumuimbila
Analidalitsa banja
Ndicho chinthu choyeletsedwa pamaso pake
Koma nthawi zina timalephera
Kugwiritsa ntchito zinthuzi
Ndipo izo zimawoneka ngati zoyipa
Ambiri tili kulephera
Kugwiritsa ntchito zinthuzi
Ndipo izo zimawoneka ngati zoyipa
Anthu achiwelewele
Amapita ku dance ndi zolinga zoyipa
Wena kovina komweko
Amakadalitsidwa ndi uthenga wabwino
Zokondwetsa mukuwona lero
Ndi chifukwa chamaphunziro akusukulu
Wena sukulu yomweyo
Amasanduka nayo mkango kumapha wanthu
Nthawi zina timalephera
Kugwiritsa ntchito zinthuzi
Ndipo izo zimawoneka ngati zoyipa
Ambiri tili kulephera
Kugwiritsa ntchito zinthuzi
Ndipo izo zimaoneka ngati zoyipa
Bambo wa nkhanza sapeleka
Njoka kwa mwana wake m'malo mwa nsomba
Koma mwana akapupuluma
Minga yomweyo yansomba ingamuphe
Ndi udindo wa achinyamata
Kukometsa dziko la pansi likhale lokoma
Popeza zonse zolengedwa
Mulungu anaziwona kuti nzabwino
Koma nthawi zina timalephera
Kugwiritsa ntchito zinthuzi
Ndipo izo zimawoneka ngati zoyipa
Ambiri tili kulephera
Kugwiritsa ntchito zinthuzi
Ndipo izo zimawoneka ngati zoyipa
Nthawi zina timalephera
Kugwiritsa ntchito zinthuzi
Ndipo izo zimawoneka ngati zoyipa
Ambiri tili kulephera
Kugwiritsa ntchito zinthuzi
Ndipo izo zimawoneka ngati zoyipa
Nthawi zina timalephera
Kugwiritsa ntchito zinthuzi
Ndipo izo zimawoneka ngati zoyipa
Ambiri tili kulephera
Kugwiritsa ntchito zinthuzi
Ndipo izo zimawoneka ngati zoyipa
Koma nthawi zina timalephera
Kugwiritsa ntchito zinthuzi
Writer(s): Sir Paul Banda
Lyrics powered by www.musixmatch.com