Titres les plus populaires de Sir Paul Banda
Titres similaires
Crédits
INTERPRÉTATION
Sir Paul Banda
Interprète
COMPOSITION ET PAROLES
Sir Paul Banda
Composition
PRODUCTION ET INGÉNIERIE
Sir Paul Banda
Production
Paroles
Nthawi yakwana wokondedwa
Yowonetsa chi khristu
Munthu oyipa musamubwezere choipa
Kuti aphunzire zachikondi
Anali kunyoza makolo ako
Palibe kanthu ndizambuyo
Maso patsogolo mothokoza Chauta
Watichitira zazikulu
Musaweruze amzanu
Kuwopa mkwiyo wa Atate
Mulungu amawona zonse zochita wanthu
Azadziwa mwini wake
Ntchito yathu masiku ano
Tikulitse chimvano
Amayi athu tonse ndi m'modzi Malawi
Tikondane wina ndi mzake
Anatisambula tikabwezere
Maganizo achikunja
Musamulore inu satana atenge mitima yanu
Mudzasanduka akapolo
Atsogoleri athu ndi a mtendere
Ndife odala Malawi
Palibe kabwino kochokera mu kumenyana
Chizangokula chisoni
Anthu oyenda mumdima
Anawona kuwala
Yesu ndiye njira chowona ndiponso moyo
Tidzafika kuchilonjezo
Tipemphere molimba
Tithokoze Ambuye
Atisungebe moyo ndikutigawira nzeru
Tiyende mu kuwala kwake
Chikondi ndicholeza mtima
Chikondi chilibe nkhanza
Chikondi sichidzitama
Chikondi chilibe kaduka
Chikondi chilibe malire
Sitikondwa pasowa chilungamo
Chikondi chimapilira
Sichilankhula zolakwa za wena
Chikondi ndicholeza mtima
Chikondi chilibe nkhanza
Chikondi sichidzitama
Chikondi chilibe kaduka
Chikondi chilibe malire
Sitikondwa pasowa chilungamo
Chikondi chimapilira
Sichilankhula zolakwa za wena
Chikondi ndicholeza mtima
Chikondi chilibe nkhanza
Chikondi sichidzitama
Chikondi chilibe kaduka
Writer(s): Sir Paul Banda
Lyrics powered by www.musixmatch.com