album cover
Mabala
754
Reggae
Mabala은(는) {albumName} 앨범에 수록된 곡으로 2012년 10월 29일일에 Malawi Goodlife에서 발매되었습니다.Son of the Poor Man
album cover
발매일2012년 10월 29일
라벨Malawi Goodlife
언어독일어
멜로디에 강한 음악
어쿠스틱 악기 중심
발랑스
춤추기 좋은 음악
에너지
BPM160

가사

Panali anthu ena wongovutika
Pamene anthu ena amkangokondwera
Panalia anthu ena wogwira ntchito
Pamene anthu ena amkangodyelera
Malume ndalama kubisa ku bank
Pamene mbumba yanu ikufa ndi njala
Koma zowuluka zonse zitawuluka
Pali tsiku limodzi zitadzatele
Inu mumati zidzakhala choncho
Mpaka liti abale?
Ana a Mulungu sangakhale akulira
Masiku onse a moyo wawo
Analanda ufumu kalero
Nawupeleka kwa woyenera
Ndichani chingamulake
Mbuye Mulungu wachilungamo!
Ndi wachikondi
Tsiku la Mulungu ndi lopambana
Koma linali tsiku la masewera
Amayi kulephera kusunga banja
Koma Ambuye sanakondwere nazo
Anthu anzeru opempha chilungamo
Amkangofa monga muja zifera ntchetche
Koma zowuluka zonse zitawuluka
Pali tsiku limodzi zitadzatele
Inu mumati zidzakhala choncho
Mpaka liti abale?
Ana a Mulungu sangakhale akulira
Masiku onse a moyo wawo
Analanda ufumu kalero
Nawupeleka kwa woyenera
Ndichani chingamulake
Mbuye Mulungu wachilungamo!
Ndi wachikondi
Ukhululuke iwe nzanga ofedwa
Puputa misozi tiyiwale zonse
Nyali yawala nkhuku ija yathawa
Tisangalare poti Mbuye watikumbuka
Zokulipa diso izo siyani
Zikanatero bwezi tonse tili a khungu
Kukhululuka ndiye ndakhululuka
Koma mabalawa ndiye akupweteka
Inu mumati zidzakhala choncho
Mpaka liti abale?
Ana a Mulungu sangakhale akulira
Masiku onse a moyo wawo
Analanda ufumu kalero
Nawupeleka kwa woyenera
Ndichani chingamulake
Mbuye Mulungu wachilungamo!
Inu mumati zidzakhala choncho
Mpaka liti abale?
Ana a Mulungu sangakhale akulira
Masiku onse a moyo wawo
Analanda ufumu kalero
Nawupeleka kwa woyenera
Ndichani chingamulake
Mbuye Mulungu wachilungamo!
Inu mumati zidzakhala choncho
Mpaka liti abale?
Ana a Mulungu sangakhale akulira
Masiku onse a moyo wawo
Analanda ufumu kalero
Nawupeleka kwa woyenera
Ndichani chingamulake
Mbuye Mulungu wachilungamo!
Inu mumati zidzakhala choncho
Mpaka liti abale?
Ana a Mulungu sangakhale akulira
Masiku onse a moyo wawo
Written by: Lucius Banda
instagramSharePathic_arrow_out􀆄 copy􀐅􀋲

Loading...