album cover
Dear Mama
album cover
Dear Mama was released on February 4, 2022 by 3767216 Records DK as a part of the album Le$$On$
AlbumLe$$On$
ReleasedFebruary 4, 2022
Label3767216 Records DK
LanguageEnglish
BPM84
Melodicness
Acousticness
Valence
Danceability
Energy

Lyrics

Dear mama, munandipatsa dzina lamu Bayibulo
Ndinatengera inu nkhope olo chiyankhulo
Ndikudziwa m'mandisowa
Mumandipemphelera usiku uliwonse musanagone tulo
Ndikulemba zonsezi ndili pa bed
Ndili kuchipatsala ndinabwerako ku TZ
Zibayo, mutu kuphwanya magazi, kutha
Ndinawonda sine dumtu mumkadziwa uja
Ndikale lija lomwe ndinachoka
Zambili zachitika, madalitso ndi matsoka
Kwanga mkungoyamika mphatso ya moyo wanga
Dziko ndalidziwa ine chilichonse ndapanga
Ndisowa poyambira ndikati ndipepese
Ikafika yonyowa kalatayi mundimvetse
Misonzi ingotsetseleka
Mukamandiletsa kuvaya out ndimkanyinyilika
Ndimkati mukundikhomelera
Ndimkati mumandiyesa ngati mwana mumandidelera
Mawu anu m'mutu mwangamu samandichoka
Samala mwanawe dziko lidangodzadza ndi njoka
Olo opanda kuphoda amuna amabwera okha
That is why ku school sizinkalongosoka
Ma blesser, ma landlord
Ma bank manager pano onse kulibe agotsala ndima bandage awo
Daily ndubayidwa ma jackson
Ndikumwa ma tablet ngati ma phone
Ndikaloga pa fb ndimamva chisoni
Zithuzi zanga zakale ndili shopping ku John
I remember tsiku lomwe munayimba phone
Begging me to come back home, you're waiting for me
You told me that I'm still a little baby
And I told you that you better speak to me like a lady
Two years ago came home to leave a baby
In my mind I was so convinced I was now ready
He was three months old
His dad is not known but
Take him as a gift from me, don't be alone
'Cause pano Ambuye thupi lija akulanda
N'naphunzira uhule gala ili kumanda
Tell my son I miss him, he should never be like me
He should go to school and be and engineer
Muchotseni chidwi pa ndalama asanakule
Muwuzeni moyo wapadziko sangagule
Mphuzitseni zambiri za matenda a edzi
Alimbilire sukulu asazakonde zibwezi
Ndavulaza ana ambiri m'ma college
Ndavulaza mabwana kuma cottage
Ma celeb ambiri atchukawa ndima ex
Sichinali chibwezi inali business
Now I'll die 21
I'll die so young but
Let me take this time to say that you're my number one
Mudayesetsa kundifunira zambiri zabwino
Bwezi pano ndili lawyer, bwezi ndili namwino koma
Zonse n'nazipeza, zonse ndizisiya
Ndilibe olo JSCE ndifa with no career
N'nali pachangu now I'll just be a late fool
Until next time I'll always be grateful
I'ts me
Written by: Evans Chimwala
instagramSharePathic_arrow_out􀆄 copy􀐅􀋲

Loading...