album cover
Tigwire Nchito
album cover
Tigwire Nchito was released on July 29, 2016 by Media 360 as a part of the album Ceasefire
July 29, 2016
LabelMedia 360
LanguageGerman
BPM93
Melodicness
Acousticness
Valence
Danceability
Energy

Music Video

Music Video

Lyrics

Muleke kugawana chuma
Pomwe mwini wake akali moyo
Kukhumba atangofa leroli
Mwayiwala kuti ali ndi banja
Kuyamba kale kudana
Pomwe iye akungodwala
Koma poti atadzafa mitima yake yanuyi
Mwana wake mudzamulera?
Anzanga!
Ngakhale mumutsogoze (sizanu)
Munthuyi anali ndi banja (sizanu)
Ana ake apanga chani? (sizanu)
Oh mama tigwire ntchito
Ngakhale mumutsogoze (sizanu)
Munthuyi anali ndi ana (sizanu)
Anawo apange chani? (sizanu)
Oh mama mupange zanu
Katundu wa nyumba mwini wake
Ndiye bambo, mayi ndi ana awo
Chonsecho mayi akamwalira
Katundu yense amatsala m'nyumbamo
Nanga bwanji bambo akamwalira
Katutu amachotsedwa m'nyumbamo
Chimene mukuchita mamuna akamwalira
Mkumusiya mkazi pa moto
Akuchimuna!
Ngakhale mumutsogoze (sizanu)
Munthuyi anali ndi banja (sizanu)
Banjalo lipanga chani? (sizanu)
Oh mama mugwire ntchito
Ngakhale mumutsogoze (sizanu)
Munthuyi anali ndi ana (sizanu)
Anawo apange chani? (sizanu)
Oh mama mupange zanu
Komaso pali akazi ena
Okhumudwitsanso khalidwe lawo
Awona mamuna wadwala kwambiri
Mwayamba kusamutsa katundu wina
Chisomo mamunayo akafa
Mam'mawa omwe akwatiwanso
Koma kodi nditadzafa manuna obwerayo
Ana anga adzawalera?
Mwachilungamo!
Ngakhale mumutsogoze (sizanu)
Munthuyi anali ndi banja (sizanu)
Banjalo lipanga chani? (sizanu)
Oh mama mugwire ntchito
Ngakhale mumutsogoze (sizanu)
Munthuyi anali ndi ana (sizanu)
Anawo agwire pati? (sizanu)
Oh mama mupange zanu
Ngakhale mumutsogoze (sizanu)
Munthuyi anali ndi banja (sizanu)
Banjalo lipanga chani? (sizanu)
Oh mama mugwire ntchito
Ngakhale mumutsogoze (sizanu)
Munthuyi anali ndi ana (sizanu)
Anawo apange chani? (sizanu)
Oh mama mupange zanu
Ngakhale mumutsogoze (sizanu)
Munthuyi anali ndi banja (sizanu)
Banjalo lipanga chani? (sizanu)
Oh mama mugwire ntchito
Ngakhale mumutsogoze (sizanu)
Anagwilira limodzi (sizanu)
Limodzi ndi mkazi wake (sizanu)
Oh mama mupange zanu
Ngakhale mumutsogoze (sizanu)
Analilira limodzi (sizanu)
(Oh mama mama)
Written by: Lucius Banda
instagramSharePathic_arrow_out􀆄 copy􀐅􀋲

Loading...