album cover
Mawu Anu
album cover
Mawu Anu was released on September 5, 2026 by MCN Music as a part of the album Mawu Anu - Single
September 5, 2026
LabelMCN Music
LanguageEnglish
BPM91
Melodicness
Acousticness
Valence
Danceability
Energy

Music Video

Music Video

Lyrics

M'dziko lililonse
Nthawi iliyonse
Amakhalapobe winawake
Omalankhula zam'mutu mwake kumalonjeza anthu
Pamisonkhano ya kampeni masomphenya ake
Zomwe mwanjira iliyonse
Akudziwa sizingadzachitike konse
Inde amatchuka ndikukwezedwa
Pamipando yolamulira
Inde choonadi akuchidziwa
Kuti kutakatakako ndi ndalama
Zomwe akuzifuna
Osati kusangalatsa kapena
Kuwatumikira anthu mwachoonadi
Kuyiwala kuti mudyamakoko
Samayiwala
Inde kumamanga nyumba m'nchenga
Malo olimba akuwaona
Mvula ndi mphepo ikaomba
Zonse n'kulakatika koopsa
Wakulichete kutsetselekha
Anthu ankawayesa wopusa aja n'kumaonelela
Kumangidwa ndi kutha kwa olonjeza chitukuko aja
M'banva zakuba masanasana
Choonadi chipambana mipando
Mawu anu apambana maufumu
Pangano lanu
Liposa zonse
Indedi ngakhale
Mitundu ingaukilane
Maufumu angagwe
Koma Mawu anu Ambuye
Adzakhalabe mpaka kalekale
Ambuye ife taona
Mafumu akubwera ena akuchoka
Maufumu akukwera ena akugwa
Aakulu ndi akale aja mayina
Lero ndi mbiri yadzana
Koma inu simusintha
Lonjezo lanu simuswa
Mpaka muyaya tidzasimba
Musaiwale padzana pajanso
Kuchokera ku mapiri atabwera ankhondo
Moto wachiopsezo
M'miyendo ndi m'maso mwawo
Panalibe mfumu yopikisana nawo
Dziko linagwedezeka chifukwa cha mphamvu zawo
Koma funso likadalipo mpaka lero
Kupyola mibadwo nyengo ndi nthawi yonseyo
Kodi mphamvu zawo
Anazigonjetsa ndani
Ngati ntchito ya manja awo
Pakuti Inu simunthu woti n'kunama
Kapena mwana wa munthu uja
Yemwe amasintha mawanga
Zimene munanena mudzazikwaniritsa
Lonjezo lililonse lidzayima mpaka muyaya
Choonadi chipambana mipando
Mawu anu apambana maufumu
Pangano lanu
Liposa zonse
Indedi ngakhale
Mitundu ingaukilane
Maufumu angagwe
Koma Mawu anu Ambuye
Adzakhalabe mpaka kalekale
Ndi Abrahamu munalonjezana
Mukuwala kwa nyenyezi za kumwamba
Lonjezo losatha munampatsa
Lomwe imfa singathe kulichotsa
Ngakhale anthu akaikire
Ngakhale chikaiko agawane
Pangano lanu lidzaimabe
Nthawi zonse silisintha konse
Mulungu akhale woona
Munthu akhale wabodza
Sitidzagwadira moto wina
Yehova basi Mulungu wathu yekha
Mulungu akhale woona
Munthu akhale wabodza
Mawu anu tidzakhulupirira
Mpaka muyaya tidzayimba
Choonadi chipambana mipando
Mawu anu apambana maufumu
Pangano lanu
Liposa zonse
Indedi ngakhale
Mitundu ingaukilane
Maufumu angagwe
Koma Mawu anu Ambuye
Adzakhalabe mpaka kalekale
Choonadi chipambana mipando
Mawu anu apambana maufumu
Malonjezo anu adzamveka
Kwamuyaya sadzatha
Pa mawu anu tidzaima
Osagwedezeka osapindika
Mogwirizana ndi zakumwamba
Mu chifuniro chanu tili limodzi
Choonadi chipambana
Mawu anu sadzatha
Maufumu onse angagwe
Koma Inu mudzakhalapobe
Samene amalankhula mokweza
Amenedi ali ndi mphamvu
Koma amene ayima pa Chowonadi
Written by: Maurice Nyasulu
instagramSharePathic_arrow_out􀆄 copy􀐅􀋲

Loading...